Patsinde
Dziwani Zaine
Tithandizane
Malo Ena
Zogawana

Kunyadila zachiMalawi

Kumbu' Kuntiya with a kid in Mangochi


Dziwani zamalo ano (kkps)

Chiyambi

Takulandilani kugawo lachitatu lantchito yanga yomwe maziko ake akuchokera kuchaka cha 2001. Nthawi imeneyo, malo ano anali anga okha, koma popita nthawi, ndidakhala ndi maganizo ena ofuna kufikila anthu ena. Izi zidapangitsa kutsegula khomo lamalo ano kwa anhu enanso kuti mwina limodzi tingatukule dziko lathu pamodzi kudzera m'makina a kompiyuta. Zolinga zanga patchito zatsamila pa izi:


  • Kufuna kudziwitsa achinyamata omwe ali pasukulu zaubwino wa makina a kompiyuta ndi intaneti.
  • kufuna kuthandizapo kupitsa potsogolo zachitukuko chadziko ndi chuma kupoyolera maphunziro a kompiyuta
khalani omasuka pogwiritsa ntchito zomwe zaikidwa pamalo pano. ndipo ngati mungafune kutengapo gawo lina lazambili zapamalo pano, khalani omasuka pogawana nane maganizo anu. 

 

 

 

Mwana wanga Natasha  (Tasha) 

Natasha Kuntiya

Dziwani za Kumbu' Kuntiya

Kumbukani kapena kuti Kumbu' momwe amzanga amanditchulira ndinaphunzirapo pasukulu ya ukachenjede  ya Tchansala ku Zomba m'chaka chapakati pa 1991 mpaka 1996 ndiponso chaka cha 1999 mpaka 2000. Padakali pano ndili pagawo lija amati Masitazi (Masters) pasukulu yaudotolo ku Blantyre. Ikakhala nkhani yantchito, ndikugwira ndi bungwe lamatchalitchi la Evangelical Association of Malawi mumzinda wa Lilongwe paudindo wa mkulu woyendetsa chilanginizo chofuna kupititsa miyoyo ya anthu odwalira kunyumba pogwiritsa ntchito matelefoni am'manja m'boma la Mangochi.

Nthawi zina ndimayendetsa ntchito za kampani ya banja lathu (Tasha Communications) pamodzi ndi mwana wanga Natasha pamodzi ndi mayi ake.

Zotetezedwa © 2001 - 2008 Tasha Communications

Zolembedwa zonse ndizotetezedwa. Muli ololedwa kugwiritsa ntchito magawo onse amalo ano posasowa chilolezo china chili chonse koma mukupemphedwa kunena komwe mwazitenga ku Tasha Communications.

Hosted by www.Geocities.ws

1